2 Chronicles 1:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuwonjezera pamenepo, guwa lamkuŵa limene adaapanga Bazalele mwana wa Uri, mwana wa Huri, linali komweko kumaso kwa chihema cha Chauta. Ndipo Solomoni adakapembedza kumeneko pamodzi ndi msonkhano wonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezalele mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la Kachisi wa Yehova; ndipo Solomoni ndi khamulo anafunako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma guwa lansembe lamkuwa limene Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri analipanga linali ku Gibiyoni kutsogolo kwa tenti ya Yehova. Kotero kuti Solomoni ndi gulu lonse anakapembedza kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezaleli mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la kacisi wa Yehova; ndipo Solomo ndi khamulo anafunako.