2 Chronicles 1:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni adati, “Inu Mulungu, mudaonetsa chikondi chanu chachikulu ndi chosasinthika kwa bambo wanga Davide, ndipo tsono mwandiika ine kuti ndikhale mfumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Solomoni kwa Mulungu, Mwachitira Davide atate wanga zokoma zambiri, ndipo mwandiika mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anayankha Mulungu kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwakukulu kwa Davide abambo anga ndipo mwayika ine kukhala mfumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Solomo kwa Mulungu, Mwacitira Davide atate wanga zokoma zambiri, ndipo mwandiika mfumu m'malo mwace.