2 Chronicles 10:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
nilankhula potsata malangizo a anyamata anzake, nkunena kuti, “Bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, koma ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nalankhula nao monga umo anampangira achinyamata, ndi kuti, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatsatira malangizo a anyamata ndipo anati, “Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nalankhula nao monga umo anampangira acinyamata, ndi kuti, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.