2 Chronicles 10:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho mfumuyo sidamvere pempho la anthuwo, pakuti Mulungu anali atazikonzeratu zinthuzo kuti zichitikedi zimene Chauta adaalankhula ndi Yerobowamu, mwana wa Nebati, kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo mfumu siinamvera anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ake, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero mfumu sinamvere anthuwo, pakuti zinthu izi zinali zochokera kwa Mulungu, kukwaniritsa mawu amene Yehova ananena kwa Yeroboamu mwana wa Nebati kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo mfumu siinamvera anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ace, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobiamu mwana wa Nebati.