2 Chronicles 10:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraele onsewo ataona kuti mfumu sidamvere zimene ankapemphazo, adayankha kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanjinso m'banja la Davide? Sitingayembekeze choloŵa chilichonse m'banja la mwana wa Yese. Ndiye inu Aisraele, bwererani kumahema kwanu. Tsopano iwe mwana wa Davide, udziwonere wekha pa banja lako.” Choncho Aisraele onsewo adachoka napita ku nyumba zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu sinawamvera anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu, Aisraele inu; yang'anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisraele onse anamuka ku mahema ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli onse ataona kuti mfumu yakana kuwamvera, iwo anayankha mfumu kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanji mwa Davide, gawo lanji mwa mwana wa Yese? Inu Aisraeli! Pitani kwanu. Iwe Davide! Yangʼana banja lako.” Kotero Aisraeli onse anapita kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuona Aisrayeli onse kuti mfumu sinawamvera anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tiri naye ciani Davide? inde tiribe colowa m'mwana wa Jese; tiyeni kwathu, Aisrayeli inu; yang'anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisrayeli onse anamuka ku mahema ao.