2 Chronicles 10:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu Rehobowamu adatuma Adoramu amene ankayang'anira ntchito yathangata, koma anthu a ku Israele adamponya miyala mpaka kumupha. Pamenepo, mfumu Rehobowamu adakwera msangamsanga pa galeta lake nathaŵira ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Rehobowamu mfumu inatuma Hadoramu woyang'anira thangata; koma ana a Israele anamponya miyala, nafa. Ndipo Rehobowamu mfumu anafulumira kukwera pa galeta wake kuthawira ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Rehobowamu inatuma Hadoramu amene ankayangʼanira ntchito yathangata, koma Aisraeli anamugenda miyala ndi kumupha. Koma mfumu Rehobowamu anakwera galeta lake ndi kuthawira ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Rehabiamu mfumu inatuma Hadoramu woyang'anira thangata; koma ana a Israyeli anamponya miyala, nafa. Ndipo Rehabiamu mfumu anafulumira kukwera pa gareta wace kuthawira ku Yerusalemu.