2 Chronicles 10:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Bambo wanu ankatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri. Ndiye ife tikuti inu tsopano mudzatipeputsireko goli lolemetsalo ndi ntchito zoŵaŵa zimene bambo wanu adatisenzetsa, apo ife tidzakutumikirani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atate wanu analemeretsa goli lathu; inu tsono pepuzaniko ntchito yolemetsa ya atate wanu, ndi goli lake lolemera anatisenzetsali, ndipo tidzakutumikirani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma tsopano mutipeputsire ntchito yolemetsayi ndi goli lolemerali limene analiyika pa ife ndipo ifeyo tidzakutumikirani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atate wanu analemeretsa goli lathu; inu tsono pepuzaniko nchito yolemetsa ya atate wanu, ndi goli lace lolemera anatisenzetsali, ndipo tidzakutumikirani.