2 Chronicles 10:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu Rehobowamu adapempha nzeru kwa madoda amene ankakhala ndi bambo wake Solomoni ndi kumamlangiza akali moyo. Adaŵafunsa kuti, “Inu mungandilangize zotani kuti ndiŵayankhe anthu ameneŵa?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Rehobowamu mfumu anafunsana ndi akuluakulu, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake akali ndi moyo, nati, Mundipangire bwanji, kuti ndiwabwezere mau anthu awa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mfumu Rehobowamu anafunsira nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira abambo ake, Solomoni, pamene anali moyo. Iye anafunsa kuti, “Kodi inu mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu awa?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Rehabiamu mfumu anafunsana ndi akulu akulu, amene anaimirira pamaso pa Solomo atate wace akali ndi moyo, nati, Mundipangire bwanji, kuti ndiwabwezere mau anthu awa?