2 Chronicles 11:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaikamo zishango ndi mikondo, ndipo adaitchinjiriza kwambiri mizindayo. Choncho ankalamulira anthu a ku Yuda ndi a ku Benjamini.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi m'midzi iliyonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa chilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmizinda yonse anayikamo zishango zikuluzikulu ndi mikondo, ndipo anachititsa kuti mizindayo ikhale yamphamvu. Choncho iye amalamulira Yuda ndi Benjamini.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi m'midzi iri yonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa cilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ace.