2 Chronicles 11:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alevi adasiya mabusa ao ndi maiko ao, ndipo adapita ku Yuda ndi ku Yerusalemu, chifukwa chakuti Yerobowamu ndi ana ake anali ataŵachotsa pa ntchito zao zaunsembe zomatumikira Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko aoao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobowamu ndi ana ake anawataya, kuti asachitire Yehova ntchito ya nsembe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi anasiya malo awo owetera ziweto ndi katundu wawo, ndi kubwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu chifukwa Yeroboamu ndi ana ake anawakana kukhala ansembe a Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko ao ao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobiamu ndi ana ace anawataya, kuti asacitire Yehova nchito ya nsembe;