2 Chronicles 11:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mwanzeru adaika ena mwa ana ake aamuna m'zigawo zonse za ku Yuda ndi za ku Benjamini, ku mizinda yonse yamalinga. Ankaŵapatsa chakudya chambiri ndi kuŵafunira akazi ochuluka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachita mwanzeru, nabalalitsa ana ake amuna onse m'maiko onse a Yuda ndi Benjamini, kumidzi yonse yamalinga; nawapatsa chakudya chochuluka, nawafunira akazi ochuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachita mwanzeru, pomwaza ena mwa ana ake ku madera onse a Yuda ndi Benjamini, ndi ku mizinda yonse yotetezedwa. Iye anawapatsa zinthu zambiri ndiponso anawafunira akazi ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacita mwanzeru, nabalalitsa ana ace amuna onse m'maiko onse a Yuda ndi Benjamini, ku midzi yonse yamalinga; nawapatsa cakudya cocuruka, nawafunira akazi ocuruka.