2 Chronicles 12:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Rehobowamu adakhazikitsa ufumu wake ku Yerusalemu. Anali wa zaka 41 nthaŵi imene ankayamba kulamulira. Adalamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Chauta adausankha pakati pa mafuko onse a Israele kuti azimpembedza kumeneko. Mai wake anali Naama, Mwamoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nadzilimbitsa Rehobowamu mfumu m'Yerusalemu, nachita ufumu; pakuti Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, ndiwo mudzi Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele, kuikapo dzina lake; ndipo dzina la make ndiye Naama Mwamoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Rehobowamu anayika maziko a ufumu wake mwamphamvu mu Yerusalemu ndipo anapitirira kukhala mfumu. Iye anali ndi zaka 41 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka 17 mu Yerusalemu, mzinda wa Yehova umene anasankha pakati pa mafuko a Aisraeli mmene Yehova anakhazikikamo. Dzina la amayi ake linali Naama, amene anali Mwamoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nadzilimbitsa Rehabiamu mfumu m'Yerusalemu, nacita ufumu; pakuti Rehabiamu anali wa zaka makumi anai mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, ndiwo mudzi Yehova adausankha m'mafuko onse a Israyeli, kuikapo dzina lace; ndipo dzina la mace ndiye Naama M-amoni.