2 Chronicles 12:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito za Rehobowamu kuyambira poyamba mpaka pomaliza, paja zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Semaya ndiponso m'buku la mbiri ya mneneri Ido. Panali nkhondo zosakata pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Machitidwe ake tsono a Rehobowamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchito za Rehobowamu, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri la mneneri Semaya ndi mlosi Ido amene amalemba mbiri? Panali nkhondo yosatha pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Macitidwe ace tsono a Rehabiamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizilembedwa kodi m'buku la mau a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehabiamu ndi Yerobiamu masiku onse.