2 Chronicles 12:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mneneri Semaya adadza kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a ku Yuda, amene anali atasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisake, ndipo adaŵauza kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Inu mwandisiya Ine, ndiye nanenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisake.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Semaya mneneri anadza kwa Rehobowamu, ndi kwa akalonga a Yuda, atasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisake, nati nao, Atero Yehova, Inu mwandisiya Ine, chifukwa chake Inenso ndasiya inu m'dzanja la Sisake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mneneri Semaya anabwera kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a Yuda amene anasonkhana mu Yerusalemu chifukwa cha Sisaki ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova akuti, ‘Inu mwandisiya, choncho Inenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisaki.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Semaya mneneri anadza kwa Rehabiamu, ndi kwa akalonga a Yuda, atasonkhana ku Yerusalemu cifukwa ca Sisaki, nati nao, Atero Yehova, Inu mwandisiya Ine, cifukwa cace Inenso ndasiya inu m'dzanja la Sisaki.