2 Chronicles 12:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta ataona kuti anthuwo adzichepetsa, adauzanso Semaya kuti, “Anthuŵa adzichepetsa, sindidzaŵaononga ai, koma ndidzaŵapulumutsa. Sindidzaukwiyira mzinda wa Yerusalemu, motero Sisake sadzauwononga konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzichepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzichepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa chipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova ataona kuti adzichepetsa, anayankhula ndi Semaya kuti, “Pakuti adzichepetsa, Ine sindiwawononga koma posachedwapa ndiwapulumutsa. Sinditsanulira ukali wanga pa Yerusalemu kudzera mwa Sisaki.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzicepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzicepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa cipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisaki.