2 Chronicles 12:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Sisake, mfumu ya ku Ejipito, adabwera kudzathira Yerusalemu nkhondo. Adalanda chuma cha ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi chuma cha ku nyumba ya mfumu. Adatenga zonse, ngakhalenso zishango zomwe zagolide zimene Solomoni adaapanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Sisake mfumu ya Aejipito anakwerera Yerusalemu, nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; anazichotsa zonse; anachotsanso zikopa zagolide adazipanga Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sisaki mfumu ya dziko la Igupto atathira nkhondo Yerusalemu, iye anatenga chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu. Iye anatenga zinthu zonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomoni anapanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Sisaki mfumu ya Aigupto anakwerera Yerusalemu, nacotsa cuma ca m'nyumba ya Yehova, ndi cuma ca m'nyumba ya mfumu; anazicotsa zonse; anacotsanso zikopa zagolidi adazipanga Solomo.