2 Chronicles 13:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo amapereka kwa Chauta nsembe zopsereza m'maŵa mulimonse ndi madzulo aliwonse. Amafukiza lubani wonunkhira bwino, amaikanso buledi wopereka pa tebulo la golide weniweni, namasamala zoikapo nyale zagolide, kuti nyale zake ziziyaka madzulo aliwonse. Ife timasunga zimene Chauta Mulungu wathu amatilamula, koma inuyo mudamsiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikapo nyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa uliwonse ndi madzulo aliwonse amapereka nsembe zopsereza ndi kufukiza lubani kwa Yehova. Iwo amayika buledi pa tebulo loyeretsedwa monga mwa mwambo ndipo amayatsa nyale pa zoyikapo nyale zagolide madzulo aliwonse. Ife timachita zofuna za Yehova Mulungu wathu. Koma inu mwamusiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za pfungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi coikapo nyali cagolidi ndi nyali zace, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga cilangizo ca Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.