2 Chronicles 13:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo anthu a ku Yuda adafuula, kufuula kwake kwankhondo. Ndipo anthu a ku Yudawo atafuula, Mulungu adagonjetsa Yerobowamu pamodzi ndi anthu a ku Israele onse, pamaso pa Abiya ndi pa anthu a ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo amuna a Yuda anafuula chokweza; ndipo pofuula amuna a Yuda, kunachitika kuti Mulungu anakantha Yerobowamu ndi Aisraele onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo asilikali a Yuda anafuwula mawu ankhondo. Atafuwula mawu ankhondowo, Mulungu anagonjetsa Yeroboamu pamodzi ndi Aisraeli onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo amuna a Yuda anapfuula cokweza; ndipo popfuula amuna a Yuda, kunacitika kuti Mulungu anakantha Yerobiamu ndi Aisrayeli onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.