2 Chronicles 13:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsopano inu mukuganiza zolimbana ndi ufumu wa Chauta ndi kuulanda m'manja mwa ana a Davide, poti inuyo ndinu ambirimbiri. Ndipo muli nawo mafano agolide, a anaang'ombe amene Yerobowamu adakupangirani, kuti akhale milungu yanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu anaang'ombe agolide adawapanga Yerobowamu akhale milungu yanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo tsopano inu mwakonzekera kutsutsana ndi ufumu wa Yehova, umene uli mʼmanja mwa zidzukulu za Davide. Inu ndithu mulipo ankhondo ambirimbiri ndipo muli ndi ana angʼombe agolide amene Yeroboamu anapanga kuti akhale milungu yanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu ana a ng'ombe agolidi adawapanga Yerobiamu akhale milungu yanu.