2 Chronicles 13:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi inu simudapirikitsa ansembe a Chauta, ana a Aaroni, ndiponso Alevi, ndipo mudadzisankhira ansembe anuanu, monga amachitira anthu a mitundu ina am'maikomo? Munthu aliyense amene amabwera kuti adzipereke atatenga mwanawang'ombe wamphongo kapena nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, amasanduka wansembe wa zinthu zimene sizili milungu konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Simunapirikitsa kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amachita anthu a m'maiko ena? Kuti aliyense wakudza kudzipatulira ndi mwanawang'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kodi inu simunathamangitse ansembe a Yehova, ana a Aaroni ndiponso Alevi ndi kudzisankhira ansembe anuanu monga anthu ena amachitira? Aliyense amene amabwera kuti adzipatule atatenga mwana wangʼombe wamwamuna ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri amakhala wansembe wa zinthu zimene sizili milungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Simunapitikitsa kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amacita anthu a m'maiko ena? kuti ali yense wakudza kudzipatulira ndi mwana wa ng'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu.