2 Chronicles 14:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Abiya adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Pambuyo pake Asa mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Pa masiku a Asa, dziko lidakhala pa mtendere zaka khumi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo Abiya anagona ndi makolo ake, ndipo anamuika m'mudzi wa Davide; ndi Asa mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake; m'masiku ake dziko linaona bata zaka khumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Abiya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide. Asa mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake ndipo pa masiku ake, dziko linakhala pa mtendere kwa zaka khumi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo Abiya anagona ndi makolo ace, ndipo anamuika m'mudzi wa Davide; ndi Asa mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace, m'masiku ace dziko linaona bata zaka khumi.