2 Chronicles 14:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Asa adafuula kwa Chauta, Mulungu wake, kuti, “Inu Chauta, palibe wina wofanafana nanu woti angathandize pakati pa anthu amphamvu ndi ofooka. Tithandizeni, Inu Chauta, Mulungu wathu, popeza kuti timakhulupirira Inu, ndipo tabwera kudzamenyana ndi chinamtindi cha anthu chimenechi m'dzina lanu. Inu Chauta, ndinu Mulungu wathu. Munthu asakupambaneni ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Asa anafuulira kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, tatulukira aunyinji awa m'dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakukanikeni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Asa anafuwulira Yehova Mulungu wake ndipo anati “Yehova palibe wina wofanana nanu kuti angathandize anthu opanda mphamvu pakati pa amphamvu. Tithandizeni Inu Yehova Mulungu wathu pakuti ife timadalira Inu ndipo mʼdzina lanu ife tabwera kudzalimbana ndi gulu la ankhondo lalikulu kwambiri ngati ili. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu, musalole kuti munthu akupambaneni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Asa anapfuulira kwa Yehova Mulungu wace, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, taturukira aunyinji awa m'dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakulakeni.