2 Chronicles 14:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asa pamodzi ndi anthu ake aja adaŵathamangitsa mpaka ku Gerari, ndipo anthu a ku Etiopiyawo adaphedwa onse, osatsalapo ndi mmodzi yemwe wamoyo. Zidatero chifukwa anali ndi mantha aakulu pamaso pa Chauta ndi gulu lake lankhondo. Ndipo Ayuda adatenga zofunkha zambirimbiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ake; ndipo anatenga zofunkha zambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo Asa ndi ankhondo ake anawathamangitsa mpaka ku Gerari. Gulu lonse lalikulu lija la Akusi linaphedwa. Sanapezeke mmodzi wamoyo pakati pawo. Iwo anakanthidwa pamaso pa Yehova ndi asilikali ake. Anthu a ku Yuda anatenga katundu wambiri olanda ku nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ace; ndipo anatenga zofunkha zambiri.