2 Chronicles 14:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamanga mizinda yamalinga ku Yuda, chifukwa dzikolo linali pa mtendere. Sadamenye nkhondo masiku amenewo, popeza kuti Chauta adampatsa mtendere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamanga midzi yamalinga m'Yuda; pakuti dziko linachita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asa anamanga mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda pakuti dziko linali pa mtendere. Panalibe amene anachita naye nkhondo mʼzaka zimenezo, pakuti Yehova anamupatsa mpumulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamanga midzi yamalinga m'Yuda; pakuti dziko linacita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.