2 Chronicles 14:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adauza anthu a ku Yuda kuti, “Tiyeni timange mizinda imeneyi, ndipo timange makoma ndi nsanja, zitseko ndi mipiringidzo yake. Dzikoli lidakali lathu, chifukwa chakuti tachita kufuna kwa Chauta, Mulungu wathu. Tachita kufuna kwake, ndipo Iye watipatsa mtendere pa mbali iliyonse.” Choncho adamangadi zimenezo, ndipo adapeza bwino ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa Yuda, Timange midzi iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosavutika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati kwa Yuda “Tiyeni timange mizinda iyi ndipo timange makoma ndi nsanja, zitseko ndi zotchinga. Dzikoli likanali lathu chifukwa tafuna Yehova Mulungu wathu; tinamufuna Iye ndipo watipatsa mpumulo mbali zonse.” Kotero iwo anamanga ndi kukhala pa ulemerero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa Yuda, Timange midzi iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosabvutika.