2 Chronicles 14:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Asa anali nalo gulu lankhondo la anthu 300,000 a ku Yuda. Iwoŵa anali ndi zishango ndi mikondo. Anthu a ku Benjamini analipo 280,000. Iwowo anali ndi zishango ndi mauta. Anthu onsewo anali amphamvu ndi olimba mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a m'Yuda zikwi mazana atatu; ndi a m'Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asa anali ndi ankhondo 300,000 ochokera ku Yuda, okhala ndi zishango zikuluzikulu ndi mikondo, ndiponso ankhondo 280,000 ochokera ku Benjamini, okhala ndi zishango ndi mauta. Onsewa anali ankhondo amphamvu ndi olimba mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika