2 Chronicles 14:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zera wa ku Etiopiya adanyamuka kukamenyana ndi Ayuda atatenga gulu lake lankhondo la anthu 1,000,000, ndi magaleta 300, ndipo adakafika mpaka ku Maresa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawatulukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi chikwi chimodzi, ndi magaleta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zera wa ku Kusi anapita kukamenyana nawo ali ndi gulu lalikulu kwambiri la asilikali ndi magaleta 300 ndipo anafika mpaka ku Maresa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anawaturukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi cikwi cimodzi, ndi magareta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.