2 Chronicles 15:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo anthu onse a ku Yuda adakondwa pa mwambo wolumbirirawo, pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse. Ankafunafuna Chauta kwambiri, ndipo adampezadi. Motero Chauta adaŵapatsa mtendere ponse poŵazungulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi chifuno chao chonse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse a ku Yuda anakondwera pa kulumbirako chifukwa analumbira ndi mtima wawo wonse. Iwo anafunafuna Mulungu mwachidwi, ndipo anamupeza Iye. Kotero Yehova anawapatsa mpumulo mbali zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi cifuno cao conse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.