2 Chronicles 15:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Asa adachotsa ngakhale ufumu wa Maaka, gogo wake, chifukwa choti Maakayo anali atachita chinthu choipa kwambiri popanga fano. Asa adagwetsa fanolo, nalitswanya, ndipo adakalitentha ku mtsinje wa Kidroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Maaka yemwe, mai wake wa Asa, mfumu, namchotsa uyu asakhalenso mai wa ufumu, popeza anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fanizolo, naliphwanyaphwanya, nalitenthera ku mtsinje wa Kidroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Asa anachotsanso Maaka agogo ake pa udindo wa amayi a mfumu chifukwa anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo, naliswa ndipo kenaka anakaliwotcha ku chigwa cha Kidroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maaka yemwe, mai wace wa Asa, mfumu, anamcotsa uyu asakhalenso mai wa ufumu, popeza anapanga fano loopsa la Asera; ndipo Asa analikha fano lace, naliphwanyaphwanya, nalitenthera ku mtsinje wa Kedroni.