2 Chronicles 15:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iye adatuluka mu mzinda wake kukakomana ndi Asa, ndipo adamuuza kuti, “Ndimvereni inu Asa, Ayuda nonsenu ndi inu Abenjamini. Chauta ali nanu nthaŵi yonse imene inu muli ndi Iye. Mukamfunafuna mudzampeza. Koma mukamsiya, nayenso adzakusiyani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapita kukakumana ndi Asa ndipo anati kwa iye, “Tandimverani, inu Asa ndi Ayuda onse ndi Benjamini. Yehova ali ndi inu, inunso mukakhala naye. Ngati inu mumufunafuna Iye mudzamupeza, koma ngati mumusiya, Iye adzakusiyani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo anaturuka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.