2 Chronicles 15:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku amenewo panalibe mtendere kwa munthu amene ankatuluka kapena kuloŵa, pakuti mavuto adaaŵagwera onse amene ankakhala m'makomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakutuluka, kapena kwa iye wakulowa, koma mavuto aakulu anagwera onse okhala m'maikomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masiku amenewo sikunali kwabwino kuyenda ulendo, pakuti anthu onse okhala mʼdziko anali pa mavuto aakulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakuturuka, kapena kwa iye wakulowa, koma mabvuto akuru anagwera onse okhala m'maikomo.