2 Chronicles 15:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Asa atamva mau ameneŵa, mau aulosi a Azariya mwana wa Odedi, adalimba mtima. Adachotsa mafano onyansa ku dziko lonse la Yuda ndi la Benjamini. Adachotsanso mafano ku mizinda imene adailanda ku dziko lamapiri la Efuremu. Ndipo adakonza guwa la Chauta limene linali patsogolo pa khonde la Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakumva Asa mau awa, ndi chinenero cha Odedi mneneriyo, analimbika mtima, nachotsa zonyansazo m'dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m'midzi adailanda ku mapiri a Efuremu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pachipinda cholowera cha nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asa atamva mawu awa ndiponso uneneri wa Azariya mwana wa Odedi, analimba mtima. Iye anachotsa mafano onse onyansa mʼdziko lonse la Yuda ndi Benjamini ndi mʼmizinda yonse imene analanda a ku mapiri a Efereimu. Iye anakonzetsa guwa lansembe la Yehova limene linali kutsogolo kwa khonde la Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakumva Asa mau awa, ndi cinenero ca Odedi mneneriyo, analimbika mtima, nacotsa zonyansazo m'dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m'midzi adailanda ku mapiri a Efraimu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pa likole la Yehova.