2 Chronicles 15:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adasonkhanitsa Ayuda onse ndi Abenjamini ndiponso anthu a ku Efuremu, Manase ndi Simeoni amene ankangokhala nao, pakuti anthu ambiri anali atathaŵira kwa mfumu Asa, kuchoka ku Israele, ataona kuti Chauta Mulungu wake anali naye Asayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namemeza onse a m'Yuda ndi m'Benjamini, ndi iwo akukhala nao ochokera ku Efuremu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ochuluka ochokera ku Israele, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wake anali naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anasonkhanitsa anthu onse a ku Yuda ndi Benjamini ndiponso anthu ochokera ku Efereimu, Manase ndi Simeoni amene ankakhala pakati pawo, pakuti gulu lalikulu linabwera kwa iye kuchokera ku Israeli litaona kuti anali ndi Yehova Mulungu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namemezaonse a m'Yuda ndi m'Benjamini, ndi iwo akukhala nao ocokera ku Efraimu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ocuruka ocokera ku Israyeli, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wace anali naye.