2 Chronicles 16:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chaka cha 36 cha ufumu wa Asa, Baasa mfumu ya ku Israele, adapita kukathira nkhondo dziko la Yuda. Adamangira linga mzinda wa Rama kuti aziletsa anthu kuloŵa kapena kutuluka m'dziko la Asa, mfumu ya ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa, Baasa mfumu ya Israele anakwera kulimbana ndi Yuda, namangitsa Rama, kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 36 cha ufumu wa Asa, Baasa mfumu ya Israeli inapita kukathira nkhondo dziko la Yuda. Anamangira mpanda mzinda wa Rama kuletsa aliyense kutuluka kapena kulowa mʼdziko la Asa mfumu ya Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi ca Asa, Basa mfumu ya Israyeli anakwera kulimbana ndi Yuda, namangitsa Rama, kuwaletsa anthu asaturuke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.