2 Chronicles 16:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chaka cha 39 cha ufumu wake, Asa adayamba kudwala nthenda ya mapazi, ndipo nthendayo idakula kwambiri. Komabe ngakhale ankadwala choncho, sadapemphe chithandizo kwa Chauta, koma kwa asing'anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu, anadwala nthenda ya mapazi, nikuladi nthendayi; koma podwala iye sanafune Yehova, koma asing'anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 39 cha ufumu wake, Asa anayamba kudwala nthenda ya mapazi. Ngakhale nthendayo inali yaululu kwambiri, komabe iye sanafunefune Yehova, koma anafuna thandizo kwa asingʼanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mpham bu zisanu ndi zitatu, anadwala nthenda ya mapazi, nikuladi nthendayi; koma podwala iye sanafuna Yehova, koma asing'anga.