2 Chronicles 16:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamuika m'manda amene iyeyo adaadzisemera mu mzinda wa Davide. Adagoneka mtembo wake pa chithatha chimene adaikapo zonunkhira zamitundumitundu zimene anthu opanga zonunkhira adazikonza. Ndipo adasonkha chimoto chachikulu kwambiri chomchitira ulemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamuika m'manda ake adadzisemerawo m'mudzi wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osanganiza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayikidwa mʼmanda amene anadzisemera yekha mu Mzinda wa Davide. Anagoneka mtembo wake pa chithatha chimene anayikapo zonunkhira zamitundumitundu, ndipo anasonkha chimoto chachikulu pomuchitira ulemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamuika m'manda ace adadzisemerawo m'mudzi wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundu mitundu, monga mwa makonzedwe a osanganiza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.