2 Chronicles 16:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Asa adatenga siliva ndi golide ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso ku nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, amene ankakhala ku Damasiko. Mau a Asa anali akuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Asa anatulutsa siliva ndi golide ku chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu; nazitumiza kwa Benihadadi mfumu ya Aramu, yokhala ku Damasiko, ndi kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Asa anatenga siliva ndi golide ku malo osungirako a mʼNyumba ya Mulungu ndi ku nyumba yake yaufumu ndi kuzitumiza kwa Beni-Hadadi mfumu ya Aramu imene inkakhala mu Damasiko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Asa anaturutsa siliva ndi golidi ku cuma ca nyumba ya Yehova, ndi ca nyumba ya mfumu; nazitumiza kwa Benihadadi mfumu ya Aramu, yokhala ku Damasiko, ndi kuti,