2 Chronicles 16:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Benihadadi adamvera zimene adanena mfumu Asa zija, motero adatuma atsogoleri a magulu ake ankhondo kukathira nkhondo mizinda ya ku Israele. Adagonjetsa Iyoni, Dani, Abele-Maimu ndi mizinda yonse ya ku Nafutali yosungiramo zinthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ake a nkhondo ayambane ndi midzi ya Israele, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Maimu, ndi midzi yonse ya chuma ya Nafutali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Beni-Hadadi anagwirizana ndi mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira nkhondo ake kukathira nkhondo mizinda ya Israeli. Iwo anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Maimu ndi mizinda yonse yosungira chuma ya Nafutali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ace a nkhondo ayambane ndi midzi ya Israyeli, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abelimaimu, ndi midzi yonse ya cuma ya Nafitali,