2 Chronicles 16:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo mneneri Hanani adadza kwa Asa mfumu ya ku Yuda, namuuza kuti, “Chifukwa chakuti mudakhulupirira mfumu ya ku Siriya, osakhulupirira Chauta, Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya ku Siriya lakuthaŵirani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, chifukwa chake khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyi mlosi Hanani anabwera kwa Asa mfumu ya Yuda ndipo anati kwa iye, “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Aramu osati Yehova Mulungu wanu, gulu la ankhondo la mfumu ya ku Aramu lapulumuka mʼmanja mwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, cifukwa cace khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.