2 Chronicles 16:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja maso a Chauta amayang'ana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi, kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wangwiro kwa Iyeyo. Inuyo mwachita zopusa pa zimenezi. Ndiye kuyambira tsopano lino, mpaka m'tsogolo muno, mudzakhala pa nkhondo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yehova amayangʼana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi kuti alimbikitse iwo amene mitima yawo ayipereka kwathunthu kwa Iye. Inu mwachita chinthu chopusa ndipo kuyambira lero mudzakhala pa nkhondo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwacita copusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.