2 Chronicles 17:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chiŵerengero chao potsata mabanja ao chinali chotere: Ku Yuda, atsogoleri a zikwi anali aŵa: Adina amene anali ndi anthu amphamvu ndi olimba mtima 300,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akulu a zikwi; Adina wamkulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chiwerengero chawo potsata mabanja awo chinali chotere: kuchokera ku Yuda, atsogoleri a magulu 1,000; mtsogoleri Adina, anali ndi anthu 300,000 odziwa nkhondo;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akuru a zikwi; Adina wamkuru, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;