2 Chronicles 17:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaika magulu ankhondo ku mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda, ndipo adamanga maboma ankhondo ku dziko la Yuda ndi ku mizinda ya ku Efuremu, imene Asa bambo wake adailanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Naika ankhondo m'midzi yonse yamalinga ya Yuda, naika aboma m'dziko la Yuda, ndi m'midzi ya Efuremu, imene adailanda Asa atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayika magulu a asilikali mʼmizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, ndipo anamanga maboma mu Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Efereimu imene Asa abambo ake analanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naika ankhondo m'midzi yonse yamalinga ya Yuda, naika aboma m'dziko la Yuda, ndi m'midzi ya Efraimu, imene adailanda Asa atate wace.