2 Chronicles 17:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta adaukhazikitsa ufumuwo m'manja mwake. Anthu onse a ku Yuda ankakhoma msonkho kwa iyeyo. Choncho anali nacho chuma chambiri ndiponso ulemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova anakhazikitsa ufumuwo m'dzanja lake, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamchulukira chuma ndi ulemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anakhazikitsa kolimba ufumuwo mʼmanja mwake ndipo Ayuda onse anabweretsa mphatso kwa Yehosafati, kotero kuti anali ndi chuma ndi ulemu wambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova anakhazikitsa ufumuwo m'dzanja lace, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamcurukira cuma ndi ulemu.