2 Chronicles 18:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina mwa iwo, Zedeki, mwana wa Kenana, adaadzisulira nyanga zachitsulo. Iyeyo adati, “Chauta akunena kuti, ‘Ndi nyangazi udzamegonjetsa Asiriya ndi kuŵaonongeratu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adatha psiti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo ndipo analengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi udzagunda Aaramu mpaka atawonongedwa!’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zacitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adatha psiti.