2 Chronicles 18:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wamthenga uja amene adaapita kukaitana Mikaya, adamuuza Mikayayo kuti, “Onani, mau onse amene akunena aneneri, akulosera mfumu zabwino. Ndiye nanunso mau anu akhale ofanafana ndi mau awo. Muzilosa zabwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu chokoma ngati m'kamwa mmodzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene chokoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wauthenga amene anapita kukayitana Mikaya anati kwa iye, “Taonani aneneri ena onse ngati munthu mmodzi akulosera za chipambano cha mfumu. Mawu anunso agwirizane ndi awo ndipo muyankhule zabwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu cokoma ngati m'kamwa m'modzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene cokoma.