2 Chronicles 18:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atafika kwa Ahabu, mfumuyo idamufunsa kuti, “Kodi Mikaya, ife tipite kukamenya nkhondo ku Ramoti-Giliyadi, kapena ineyo ndileke?” Iye adayankha kuti, “Pitani, mukapambana, anthuwo akaperekedwa kwa inu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene anafika kwa mfumu, mfumu inanena naye, Mikaya timuke ku Ramoti Giliyadi kunkhondo kodi, kapena ndileke? Nati iye, Kwerani, mudzachita mwai; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye atafika mfumu inamufunsa kuti, “Mikaya, kodi tipite ku nkhondo kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?” Iye anayankha kuti, “Kathireni nkhondo ndipo kapambaneni, pakuti mzindawo udzaperekedwa mʼdzanja lanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene anafika kwa mfumu, mfumu inanena naye, Mikaya timuke ku Ramoti Gileadi kunkhondo kodi, kapena ndileke? Nati iye, Kwerani, mudzacita mwai; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lanu.