2 Chronicles 18:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mikaya adati, “Ndidaona Aisraele onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono Chauta adati, ‘Ameneŵa alibe mbuyawo. Aliyense apite kwao mwamtendere.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; nati Yehova, Awa alibe mbuye wao, abwerere yense kunyumba yake mumtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Mikaya anayankha kuti, “Ine ndinaona Aisraeli atabalalika mʼmapiri monga nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mu mtendere!’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Ndinaona Aisrayeli onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; nati Yehova, Awa alibe mbuye wao, abwerere yense ku nyumba yace mumtendere.