2 Chronicles 18:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adati, ‘Kodi ndani amene akamnyengerere Ahabu mfumu ya ku Israele, kuti akafe ku Ramoti-Giliyadi?’ Wina ankanena zina, winanso nkumanena zina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati Yehova, Adzamnyenga Ahabu mfumu ya Israele ndani, kuti akwereko, nagwe ku Ramoti Giliyadi? Nati wina mwakuti, wina mwakuti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anati, ‘Ndani amene adzamunyengerere Ahabu mfumu ya Israeli kuti akathire nkhondo Ramoti Giliyadi ndi kukafera komweko?’ “Wina ananena zina, winanso ananena zina.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati Yehova, Adzamnyenga Ahabu mfumu ya Israyeli ndani, kuti akwereko, nagwe ku Ramoti Gileadi? Nati wina mwakuti, wina mwakuti.