2 Chronicles 18:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita zaka zina, Yehosafatiyo adapita kwa Ahabu ku Samariya. Ahabuyo adapha nkhosa ndi ng'ombe zambirimbiri kuphera Yehosafatiyo ndi anthu amene anali naye, pofuna kumkopa kuti akalimbane ndi Ramoti-Giliyadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng'ombe zochuluka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Giliyadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita zaka zina, iye anapita kukacheza kwa Ahabu mu Samariya. Ahabu anaphera iye pamodzi ndi anthu amene anali naye, nkhosa zambiri ndi ngʼombe ndipo anamuwumiriza kuti akathire nawo nkhondo Ramoti Giliyadi
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng'ombe zocuruka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Gileadi.