2 Chronicles 18:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mzimu wina udadzaima pamaso pa Chauta, nunena kuti, ‘Ndikamnyengerera ndine.’ Tsono Chauta adaufunsa kuti, ‘Ukamnyengerera bwanji?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo unatuluka mzimu, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Ndipo Yehova, ananena nao, Ndi chiyani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomaliza mzimu wina unatuluka ndi kuyima pamaso pa Yehova ndipo unati, “Ine ndikamunyengerera!” Yehova anafunsa kuti, “Ukagwiritsa ntchito njira yanji?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo unaturuka mzimu, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Ndipo Yehova, ananena nao, Ndi ciani?